Nehemiah 13:30 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Umu ndimo m'mene ndidaŵayeretsera anthu poŵachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndidakhazikitsa ntchito za ansembe ndi za Alevi, kuti aliyense adziŵe bwino ntchito yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Momwemo ndinawayeretsa kuwachotsera achilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense kuntchito yake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero ndinayeretsa ansembe ndi Alevi powachotsera kalikonse kachilendo. Ndipo ndinakhazikitsa ntchito zawo, kuti aliyense akhale pa ntchito yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Momwemo ndinawayeretsa kuwacotsera acilendo onse, ndi kuikira udikiro ansembe ndi Alevi, yense ku nchito yace;