Nehemiah 13:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
adakonzera Tobiyayo chipinda chachikulu m'mene kale ankasungiramo zopereka zaufa, lubani, ziŵiya, mphatso zoyenerera ansembe, ndiponso zopereka za chachikhumi cha chakudya, vinyo ndi mafuta, zimene adaalamula kuti azipatse Alevi, anthu oimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, potsata malamulo a Mose.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
namkonzera chipinda chachikulu, kumene adasungira kale zopereka za ufa, lubani, ndi zipangizo, ndi limodzilimodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamulidwira Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anamupatsa chipinda chachikulu chimene kale ankasungamo zopereka zakudya, lubani, ziwiya, zopereka za chakhumi za tirigu, vinyo ndi mafuta zoyenera kuperekedwa kwa Alevi, oyimba nyimbo ndi alonda a ku Nyumba ya Mulungu, komanso mphatso zoyenera kupereka kwa ansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
namkonzera cipinda cacikuru, kumene adasungira kale zopereka za ufa, libano, ndi zipangizo, ndi limodzi limodzi la magawo khumi a tirigu, vinyo, ndi mafuta, zolamutidwira Alevi, ndi oyimbira, ndi odikira, ndi nsembe zokweza za ansembe.