Nehemiah 13:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene zimenezi zinkachitika ku Yerusalemu, nkuti ine palibe, popeza kuti pa chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, mfumu ya ku Babiloni, ine ndidaapita kwa mfumuyo. Patapita nthaŵi ndithu, ndidapempha chilolezo kwa mfumu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pochitika ichi chonse sindinakhala ku Yerusalemu; pakuti chaka cha makumi atatu ndi chachiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu ya Babiloni ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene izi zonse zinkachitika mu Yerusalemu, ine kunalibe popeza mʼchaka cha 32 cha Aritasasita mfumu ya Babuloni ine ndinabwerera kwa mfumu. Patapitanso nthawi ndinapempha chilolezo kwa mfumuyo
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pocitika ici conse sindinakhala ku Yerusalemu; pakuti caka ca makumi atatu ndi caciwiri ca Aritasasta mfumu ya Babulo ndinafika kwa mfumu, ndipo atapita masiku ena ndinapempha mfumu indilole;