Nehemiah 2:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa mwezi wa Nisani, chaka cha 20 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, pamene adabwera ndi vinyo pamaso pa mfumuyo, ndidatenga vinyoyo ndi kumpereka kwa mfumu. Tsono nkale lonse sindidakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kunachitika mwezi wa Nisani, chaka cha makumi awiri cha Arita-kisereksesi mfumu pokhala vinyo pamaso pake, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wachisoni pamaso pake ndi kale lonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mwezi wa Nisani, mʼchaka cha makumi awiri cha ufumu wa Aritasasita, atabwera ndi vinyo pamaso pa mfumu ine ndinatenga vinyoyo ndi kupereka kwa mfumu. Koma ndinali ndisanakhalepo ndi nkhope yachisoni pamaso pake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kunacitika mwezi wa Nisana, caka ca makumi awiri ca Aritasasta mfumu pokhala vinyo pamaso pace, ndinatenga vinyoyo ndi kuipatsa mfumu. Koma sindidakhala wacisoni pamaso pace ndi kale lonse.