Nehemiah 2:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma atamva zimenezi, akuluakulu aŵa, Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya, mkulu wina wa chigawo cha Amoni, adaipidwa kwambiri poona kuti wina wabwera kudzachitira Aisraele zabwino.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sanibalati wa ku Horoni ndi Tobiya wa ku Amoni atamva zimenezi, iwo anayipidwa kwambiri kuti wina wabwera kudzachitira zabwino Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atamva Sanibalati Mhoroni, ndi Tobiya kapoloyo M-amoni, cidawaipira kwakukuru, kuti wadza munthu kuwafunica ana a Israyeli cokoma.