Nehemiah 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sindidauze ndi mmodzi yemwe zimene Mulungu wanga adaaika mumtima mwanga, zoti ndichitire Yerusalemu. Tsono ndidadzuka usiku pamodzi ndi anthu ena oŵerengeka. Ndinalibe bulu wina kupatula yekhayo amene ndidaakwerapo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine choika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndichitire Yerusalemu; panalibenso nyama ina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindinawuze munthu aliyense za zimene Yehova anayika mu mtima mwanga kuti ndichitire mzinda wa Yerusalemu. Choncho ndinanyamuka usiku pamodzi ndi anthu ena owerengeka. Ndinalibe bulu wina aliyense kupatula amene ndinakwerapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinauka usiku, ine ndi amuna owerengeka nane, osauza munthu yense ine coika Mulungu wanga m'mtima mwanga ndicitire Yerusalemu; panalibenso nyama yina nane, koma nyama imene ndinakhalapo.