Nehemiah 2:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa, nkuyenda cha ku Chitsime cha Chilombo Cham'madzi ndi ku Chipata cha Zinyalala. Ndipo ndidayang'ana makoma a Yerusalemu amene adaagamukagamuka ndiponso zipata zake zimene zidaaonongeka ndi moto.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinatuluka usiku podzera ku Chipata cha ku Chigwa ndi kuyenda kupita ku Chitsime cha Chirombo Chamʼmadzi mpaka ku Chipata cha Zinyalala. Ndinayangʼana makoma a Yerusalemu, amene anagwetsedwa, ndi zipata zake, zimene zinawonongedwa ndi moto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinaturuka usiku pa cipata ca kucigwa, kumka ku citsime ca cinjoka, ndi ku cipata ca kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zace zothedwa ndi moto.