Nehemiah 2:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake ndidapitirira mpaka kukafika ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziŵe la Mfumu. Koma panalibe malo oti bulu amene ndidaakwerapoyo adzerepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapitirira kunka ku Chipata cha Chitsime, ndi ku Dziwe la Mfumu; koma popita nyama ili pansi panga panaichepera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka ndinapita ku Chipata cha Kasupe ndi ku Dziwe la Mfumu. Koma panalibe malo okwanira akuti bulu wanga adutse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapitima kumka ku cipata cacitsime, ndi ku dziwe la mfumu; koma popita nyama iri pansi panga panaicepera.