Nehemiah 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akuluakulu aja sadadziŵe kumene ndidaapita kapenanso zimene ndinkachita. Ndinali ndisanaŵauze Ayuda, ansembe, atsogoleri, akuluakulu aja kapenanso ena onse amene ankayenera kudzagwira ntchitoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma olamulira sanadziwe uko ndinamuka, kapena chochita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufulu, kapena olamulira, kapena otsala akuchita ntchitoyi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu sanadziwe kumene ndinapita kapena zimene ndimachita, chifukwa pa nthawiyi nʼkuti ndisananene kalikonse kwa Ayuda kapena ansembe, anthu olemekezeka kapena akuluakulu, kapena wina aliyense amene anali woyenera kugwira ntchitoyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma olamulira sanadziwa uko ndinamuka, kapena cocita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufuru, kapena olamulira, kapena otsala akucita nchitoyi.