Nehemiah 2:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero ndidaŵasimbira za m'mene Mulungu wanga adandithandizira ndiponso mau amene mfumu idandiwuza. Apo anthuwo adati, “Tiyeni tiyambepo kumanga.” Choncho adalimbitsana mtima kuti akaiyambe ntchito yabwinoyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza. Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Cotero anandilimbitsira manja mokoma.