Nehemiah 2:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine ndidaŵayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba adzatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino, ndipo ife atumiki ake tiyambapo kumanga. Koma inuyo mulibe chanu muno, mulibe mphamvu yolandirira malo muno, ndipo mulibenso chilichonse chokumbutsa za inu mu Yerusalemu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; chifukwa chake ife akapolo ake tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena chikumbukiro, m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ndinawayankha kuti, “Mulungu Wakumwamba atithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Ife antchito ake tiyambapo kumanga. Koma inu mulibe gawo lanu muno mu Yerusalemu. Mulibe chokuyenerezani kulandira malo ano. Mulibenso chilichonse muno chokumbutsa za inu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ndinawabwezera mau, ndi kunena nao, Mulungu Wam'mwamba, Iye ndiye adzatilemeza; cifukwa cace ife akapolo ace tidzanyamuka ndi kumanga; koma inu mulibe gawo, kapena ulamuliro, kapena cikumbukilo, m'Yerusalemu.