Nehemiah 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidauza mfumu kuti, “Amfumu akhale ndi moyo mpakampaka. Ilekerenji nkhope yanga kukhala yakugwa, pamene mzinda kumene kuli manda a makolo anga, adani adausandutsa bwinja, ndipo zipata zake adazitentha ndi moto?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kuchita chisoni, popeza pali bwinja kumudzi kuli manda a makolo anga, ndi zipata zake zopsereza ndi moto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndinawuza mfumu kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wamuyaya! Kodi nkhope yanga ilekerenji kuoneka yachisoni pamene mzinda umene kuli manda a makolo anga, wasanduka bwinja ndipo zipata zake zinawonongedwa ndi moto?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinati kwa mfumu, Mfumu ikhale ndi moyo kosatha; ilekerenji nkhope yanga kucita cisoni, popeza pali bwinja kumudzi kuli manda a makolo anga, ndi zipata zace zopsereza ndi moto.