Nehemiah 2:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ndidaiwuza mfumuyo kuti, “Ngati chingakukondweretseni amfumu, ndipo ngati mungandikomere mtima mtumiki wanune, munditume ku Yuda, kumzinda kumene kuli manda a makolo anga, kuti ndikaumangenso mzindawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinati kwa mfumu, Chikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda kumudzi wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinayankha kuti, “Ngati amfumu chingakukondweretseni, ngati mungakomere mtima mtumiki wanune, mundilole kuti ndipite ku Yuda, ku mzinda kumene kuli manda a makolo anga kuti ndikawumangenso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinati kwa mfumu, Cikakomera mfumu, ndi mtima wanu ukakomera kapolo wanu, munditumize ku Yuda ku mudzi wa manda a makolo anga, kuti ndiumange.