Nehemiah 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu, mkazi wake ali pambali pake, idandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako nthaŵi yaitali bwanji, ndipo udzabwerako liti?” Ndidaiwuza nthaŵi yake, ndipo idandilola kuti ndipite.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ninena nane mfumu, ilikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wake wamkulu, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaitchula nthawi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mfumu, mfumukazi itakhala pambali pake, anandifunsa kuti, “Kodi kumeneko ukakhalako masiku angati ndipo udzabwera liti?” Ndinayiwuza mfumu nthawi yake ndipo inandilola kuti ndipite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ninena nane mfumu, irikukhala pansi pamodzi ndi mkazi wace wamkuru, Ulendo wako ngwa nthawi yanji, udzabweranso liti? Ndipo kudakonda mfumu kunditumiza nditaichula nthawi.