Nehemiah 2:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidauza mfumu kuti, “Ngati chingakukondweretseni amfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudzera m'chigawocho mpaka ndikafike ku Yuda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinanenanso kwa mfumu, Chikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ndinatinso kwa mfumu, “Ngati zikondweretse mfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a ku chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudutsa mwamtendere mpaka nditakafika ku Yuda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinanenanso kwa mfumu, Cikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda;