Nehemiah 3:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Eliyasibu, mkulu wa ansembe, adayamba kugwira ntchito pamodzi ndi ansembe anzake, ndipo adamanga Chipata cha Nkhosa. Adachipatulira Mulungu naika zitseko zake. Khoma limene adapatulalo lidafika ku Nsanja ya Zana, mpakanso ku Nsanja ya Hananele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga chipata chankhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka nsanja ya Hananele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Eliyasibu mkulu wa ansembe ndi ansembe anzake anayamba kugwira ntchito ndipo anamanganso Chipata cha Nkhosa. Iwo anachipatulira Mulungu ndipo anayika zitseko zake. Khoma limene analipatula linafika mpaka pa Nsanja ya Zana ndi Nsanja ya Hananeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Eliasibu mkuru wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ace ansembe, namanga cipata cankhosa; anacipatula, naika zitseko zace, inde anacipatula mpaka nsanja ya Mea, mpaka nsanja ya Hananeeli.