Nehemiah 3:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iwowo Yedaya, mwana wa Harumafa, adakonza chigawo choyang'anana ndi nyumba yake. Pambali pa iyeyo Hatusi, mwana wa Hasabuneiya, adakonza chigawo china.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafa, pandunji pa nyumba yake. Ndi pambali pake anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kulumikiza ichi, Yedaya mwana wa Harumafi anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba yake, ndipo Hatusi mwana wa Hasabaneya anakonzanso motsatana naye.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pambali pao anakonza Yedaya mwana wa Harumafi, pandunji pa nyumba yace. Ndi pambali pace anakonza Hatusi mwana wa Hasabineya.