Nehemiah 3:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Hanuni pamodzi ndi nzika za ku Zanowa adakonza Chipata cha ku Chigwa. Adachimanganso naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake. Adakonzanso khoma mamita 400 mpaka kukafika ku Chipata cha Zinyalala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chipata cha ku Chigwa anachikonza Hanuni; ndi okhala m'Zanowa anachimanga, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso mikono chikwi chimodzi cha lingalo mpaka ku Chipata cha Kudzala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipata cha ku chigwa chinakonzedwa ndi Hanuni ndi anthu okhala ku Zanowa. Iwo anachimanganso ndi kuyika zitseko zake ndi zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iwo anakonzanso khoma lotalika mamita 450 mpaka ku Chipata cha Zinyalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cipata ca kucigwa anacikonza Hanini; ndi okhala m'Zanowa anacimanga, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace; ndiponso mikono cikwi cimodzi ca lingalo mpaka ku cipata ca kudzala.