Nehemiah 3:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Salumu mwana wa Kolihoze wolamulira dera la Mizipa, adakonza Chipata cha Kasupe. Adachimanganso, naikira denga lake, zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Adamanganso khoma la Dziŵe la Sela pafupi ndi munda wa mfumu, mpaka ku makwerero otsikira potuluka mu mzinda wa Davide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chipata cha kukasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pa munda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumudzi wa Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipata cha Kasupe chinakonzedwa ndi Saluni mwana wa Koli-Hoze, wolamulira chigawo cha Mizipa. Iye anachimanganso ndi kuyikanso denga ndiponso zitseko, zotsekera ndi mipiringidzo yake. Iye anakonzanso khoma la Dziwe la Siloamu limene lili pafupi ndi munda wa mfumu mpaka ku makwerero otsikira potuluka mzinda wa Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cipata ca kukasupe anacikonza Saluni mwana wa Koli, Hoze mkuru wa dziko la Mizipa anacimanga, nacikomaniza pamwamba pace, naika zitseko zace, zokowera zace, ndi mipiringidzo yace; ndiponso linga la dziwe la Sela pa munda wa mfumu, ndi kufikira ku makwerero otsikira ku mudzi wa Davide.