Nehemiah 3:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iyeyo Nehemiya, mwana wa Azibuki, wolamulira theka la dera la Betezuri, adakonza chigawo china mpaka ku malo oyang'anana ndi manda a Davide, ndi kukafika ku dziŵe lokumba ndiponso ku nyumba ya ankhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkulu wa dera lake lina la dziko la Betezuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi kunyumba ya amphamvu aja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambali pa iyeyo, Nehemiya mwana wa Azibuki, wolamulira theka la chigawo cha Beti Zuri anakonza chigawo china mpaka kumalo oyangʼanana ndi manda a Davide, mpaka ku dziwe lokumba ndi ku nyumba ya anthu ankhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana naye anakonza Nehemiya mwana wa Azibuki, mkuru wa dera lace lina la dziko la Bete Zuri, mpaka malo a pandunji pa manda a Davide, ndi ku dziwe adalikumba, ndi ku nyumba ya amphamvu aja.