Nehemiah 3:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa Nehemiyayo Alevi adakonza chigawo china. Mtsogoleri wao anali Rehumu mwana wa Bani. Pambali pa iyeyo Basabiya, wolamulira theka la dera la Keila, adakonza chigawo chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pake anakonza Hasabiya mkulu wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambali pake Alevi anakonza chigawo china, ndipo mtsogoleri wawo anali Rehumi mwana wa Bani. Pambali pa iye Hasabiya wolamulira theka la chigawo cha Keyila anagwira ntchito ku chigawo chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana naye anakonza Alevi, Rehumu mwana wa Bani. Pambali pace anakonza Hasabiya mkuru wa dera lina la dziko la Keila, kukonzera dziko lace.