Nehemiah 3:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iyeyo abale ao adapitiriza kukonza. Mtsogoleri wao anali Bavai mwana wa Henadadi, wolamulira theka la dera lina la Keila.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkulu wa dera lina la dziko la Keila.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pa iyeyu abale awo anapitiriza kukonza, ndipo mtsogoleri wawo anali Bawai mwana wa Henadadi, wolamulira theka lina la chigawo cha Keyila.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana naye anakonza abale ao, Bavai mwana wa Henadadi, mkuru wa dera lina la dziko la Keila.