Nehemiah 3:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iyeyo Ezere mwana wa Yesuwa wolamulira Mizipa, adakonza chigawo china choyang'anana ndi chikweza chofikira ku malo osungira zida zankhondo pa Ndonyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pa mbali pake Ezere mwana wa Yesuwa, mkulu wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera kunyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motsatana naye Ezeri mwana wa Yesuwa, wolamulira Mizipa anakonza chigawo chinanso choyangʼanana ndi chikweza chofikira ku nyumba yosungira zida za nkhondo pa ngodya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pa mbali pace Ezeri mwana wa Yesuwa, mkuru wa Mizipa, anakonza gawo lina, pandunji pokwerera ku nyumba yosungamo zida za nkhondo, popindirira linga.