Nehemiah 3:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iyeyo Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi, adakonza chigawo china kuyambira ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka ku mathero a nyumbayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uriya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira kukhomo la nyumba ya Eliyasibu kufikira malekezero ake a nyumba ya Eliyasibu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motsatana naye, Meremoti mwana wa Uriya, mwana wa Hakozi anakonzanso chigawo china kuchokera ku chitseko cha nyumba ya Eliyasibu mpaka kumapeto kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana naye Meremoti mwana wa Uliya mwana wa Hakozi anakonza gawo lina, kuyambira ku khomo la nyumba ya Eliasibu kufikira malekezero ace a nyumba ya Eliasibu.