Nehemiah 3:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iwowo Benjamini ndi Hasubu adakonza chigawo china choyang'anana ndi nyumba zao. Pambali pa iwowo Azariya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Ananiya, adakonza chigawo china pafupi ndi nyumba yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubu pandunji pa nyumba pao. Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maaseiya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pawo, Benjamini ndi Hasubu anakonza kutsogolo kwa nyumba zawo. Ndipo motsatana nawo, Azariya mwana wa Maaseya mwana wa Ananiya, anakonza chigawo choyangʼanana ndi nyumba zawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana nao anakonza Benjamini ndi Hasubi pandunji pa nyumba pao, Potsatizana nao anakonza Azariya mwana wa Maseya mwana wa Ananiya pafupi pa nyumba yace.