Nehemiah 3:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iyeyo Binuyi, mwana wa Henadadi, adakonza chigawo china, kuyambira ku nyumba ya Azariya mpaka kukafika ku Ndonyo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana naye Binuyi mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira kunyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungodya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motsatana naye, Binuyi mwana wa Henadadi anakonzanso chigawo china, kuchokera pa nyumba ya Azariya kukafika potsirizira pa ngodya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana naye Binui mwana wa Henadadi anakonza gawo lina, kuyambira ku nyumba ya Azariya kufikira popindirira kufikira kungondya.