Nehemiah 3:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndiponso mpaka ku ngodya. Palala, mwana wa Uzai, adakonza chigawo china choyang'anana ndi Ndonyo ndiponso ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Pambali pa iyeyo Pedaya, mwana wa Parosi,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene ili kubwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Palali mwana Uzai anakonza chigawo china choyangʼanana ndi ngodya ndi nsanja yotuluka pa nyumba yapamwamba ya mfumu ku bwalo la alonda. Motsatana naye, Pedaya mwana wa Parosi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Palali mwana wa Uzai anakonza pandunji popindirira, ndi nsanja yosomphoka pa nyumba ya mfumu ya kumtunda, imene iri ku bwalo la kaidi. Potsatizana naye anakonza Pedaya mwana wa Parosi.