Nehemiah 3:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndi atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, amene ankakhala pa khoma la Ofele, adakonza chigawo china mpaka ku malo oyang'anana ndi Chipata cha Madzi kuvuma, ndiponso nsanja yaitali ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Anetini okhala m'Ofele anakonza kufikira kumalo a pandunji pa Chipata cha Madzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndi otumikira mʼNyumba ya Mulungu amene amakhala pa khoma la Ofeli anakonza chigawo china mpaka pa malo oyangʼanana ndi Chipata cha Madzi kuloza kummawa ndiponso nsanja yayitali ija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Anetini okhala m'Ofeli anakonza kufikira ku malo a pandunji pa cipata ca kumadzi kum'mawa, ndi nsanja yosomphokayo,