Nehemiah 3:27 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa Pedaya ndi anzake, Atekowa adakonza chigawo china choyang'anana ndi nsanja ija yaikulu ndi yaitali mpaka kukafika ku khoma la Ofele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana nao Atekowa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikulu yosomphoka ndi kulinga la Ofele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motsatana nawo, anthu a ku Tekowa anakonzanso chigawo china choyangʼanana ndi nsanja ija yayikulu ndi yayitali mpaka ku khoma la Ofeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana nao Atekoa anakonza gawo lina, pandunji pa nsanja yaikuru yosomphoka ndi ku linga la Ofeli.