Nehemiah 3:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iwowo Zadoki, mwana wa Imeri, adakonza chigawo china choyang'anananso ndi nyumba yake. Pambali pa iyeyo Semaya, mwana wa Sekaniya, amene ankasunga Chipata chakuvuma, adakonza chigawo china.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana nao anakonza Zadoki mwana wa Imeri pandunji pa nyumba yake. Ndi potsatizana naye anakonza Semaya mwana wa Sekaniya, wosunga chipata cha kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motsatana nawo, Zadoki mwana wa Imeri anakonza chigawo china choyangʼanana ndi nyumba yake. Motsatana naye, Semeya mwana wa Sekaniya, mlonda wa Chipata cha Kummawa, anakonzanso khoma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana nao anakonza Zadoki mwana wa Imeri pandunji pa nyumba yace. Ndi potsatizana naye anakonza Semaya mwana wa Sekaniya, wosunga cipata ca kum'mawa.