Nehemiah 3:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iyeyo Hananiya, mwana wa Selemiya, ndiponso Hanuni, mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, adakonza chigawo china. Pambali pa iwowo Mesulamu, mwana wa Berekiya, adakonza chigawo choyang'anana ndi chipinda chake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa chipinda chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Hananiya mwana wa Selemiya ndiponso Hanuni mwana wachisanu ndi chimodzi wa Zalafi anakonza chigawo china. Motsatana naye, Mesulamu mwana wa Berekiya anakonza chigawo choyangʼanana ndi chipinda chake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana naye Hananiya mwana wa Selemiya, ndi Hanuni mwana wacisanu ndi cimodzi wa Salafi, anakonza gawo lina. Potsatizana naye anakonza Mesulamu mwana wa Berekiya pandunji pa cipinda cace.