Nehemiah 3:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iyeyo Malikiya, mmodzi mwa amisiri a golide, adakonza chigawo china mpaka kukafika ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda. Chigawo chimenechi chidaayang'anana ndi Chipata cha Mifikada, kufikira ku chipinda chapamwamba chapangodya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golide kufikira kunyumba ya Anetini, ndi ya ochita malonda, pandunji pa chipata cha Hamifikadi, ndi kuchipinda chosanja cha kungodya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motsatana naye, Malikiya mmodzi mwa amisiri a golide anakonza chigawo china mpaka ku nyumba ya atumiki a ku Nyumba ya Mulungu ndiponso ku nyumba ya anthu amalonda moyangʼanana ndi chipata cha Mifikade ndiponso mpaka pa chipinda chapamwamba chapangodya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potsatizana naye anakonza Malikiya wina wa osula golidi kufikira ku nyumba ya Anetini, ndi ya ocita malonda, pandunji pa cipata ca Hamifikadi, ndi ku cipinda cosanja ca kungondya.