Nehemiah 3:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iwowo Atekowa adakonza chigawo china, koma atsogoleri ao adakana kugwira ntchito imene akuluakulu ao adaŵapatsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pambali pao anakonza Atekowa; koma omveka ao sanapereke makosi ao kuntchito ya Mbuye wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambali pa iwowa anthu a ku Tekowa anakonza chigawo china. Koma wolemekezeka awo anakana kugwira ntchito imene akuluakulu awo anawapatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pambali pao anakonza Atekoa; koma omveka ao sanapereka makosi ao ku nchito ya Mbuye wao.