Nehemiah 3:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yoyada, mwana wa Paseya, ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya, adakonza Chipata Chakale. Adayala mitanda yake naikira zitseko zake, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chipata chakale anachikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeiya anamanga mitanda yake, ndi kuika zitseko zake, ndi zokowera zake, ndi mipingiridzo yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipata cha Yesana chinakonzedwa ndi Yoyada mwana wa Paseya ndi Mesulamu mwana wa Besodeya. Iwo anayika mitanda yake ndi kuyika zitseko, zotsekera zake ndi mipiringidzo yake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi cipata cakale anacikonza Yoyada mwana wa Paseya; ndi Mesulamu mwana wa Besodeya anamanga mitanda yace, ndi kuika zitseko zace, ndi zokowera zace, ndi mipingiridzo yace.