Nehemiah 3:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iwowo Uziyele, mwana wa Haraiya, wa m'gulu la amisiri osula golide, adakonza chigawo china. Pambali pa iyeyo Hananiya, mmodzi mwa anthu oyenga mafuta onunkhira, adakonza chigawo china. Onsewo adakonza Yerusalemu mpaka ku Khoma Lotambasuka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pambali pake anakonza Uziyele mwana wa Haraya, wa iwo osula golide. Ndi padzanja pake anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lachitando.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambali pawo Uzieli mwana wa Harihaya wa mʼgulu amisiri osula golide anakonzanso chigawo china. Pambali pake Hananiya mmodzi mwa anthu oyenga mafuta onunkhira, anakonzanso chigawo china. Iwo anakonzanso Yerusalemu mpaka ku Khoma Lotambasuka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pambali pace anakonza Uziyeli mwana wa Haraya, wa iwo osula golidi. Ndi padzanja pace anakonza Hananiya, wa iwo osanganiza zonunkhira; nalimbikitsa Yerusalemu mpaka linga lacitando.