Nehemiah 3:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa iwowo Refaya, mwana wa Huri, wolamulira theka la dera la mzinda wa Yerusalemu, adakonza chigawo china.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkulu wa dera lina la dziko la Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Refaya mwana wa Huri wolamulira theka la chigawo cha Yerusalemu anakonza chigawo china motsatana nawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pambali pao anakonza Refaya mwana wa Huri, ndiye mkuru wa dera lina la dziko la Yerusalemu.