Nehemiah 4:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ayuda ankati, “Mphamvu za onyamula zinyalala zilikutha, ndipo zinyalala zoyenera kutayidwazo nzambiri. Ndiyetu sitiitha ife ntchito yomanga khomayi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi lichuluka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi yomweyi anthu a ku Yuda anati, “Mphamvu za anthu onyamula zinyalala zikutha ndipo pali zinyalala zambiri. Choncho ife sititha kumanga khomali.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ayuda anati, Mphamvu ya osenza akatundu yatha, ndi dothi licuruka, motero sitidzakhoza kumanga lingali.