Nehemiah 4:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma nditazindikira mantha ao, ndidachitapo kanthu. Mwakuti ndidauza atsogoleri ndi akulu olamula, ndiponso anthu ena onse kuti, “Musaŵaope ameneŵa. Kumbukirani kuti Chauta ndi wamkulu ndiponso ndi woopsa, tsono mumenyere nkhondo abale anu, ana anu, akazi anu, ndi nyumba zanu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukirani Yehova wamkulu ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu aamuna ndi aakazi, akazi anu, ndi nyumba zanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza anthu ankachita mantha, tsono ndinawawuza anthu olemekezeka, akuluakulu ndiponso anthu onse kuti, “Musawaope. Kumbukirani kuti Ambuye ndi wamkulu ndipo ndi woopsa. Choncho menyerani nkhondo abale anu, ana aamuna ndi aakazi, akazi anu ndi nyumba zanu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinapenya, ndinanyamuka, ndinanena kwa aufulu, ndi olamulira, ndi anthu otsala, Musamawaopa iwo; kumbukilani Yehova wamkuru ndi woopsa, ndi kuponyera nkhondo abale anu, ana anu amuna ndi akazi, akazi anu, ndi nyumba zanu.