Nehemiah 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adani athu adamva kuti ife tikudziŵa cholinga chao, adazindikira kuti Mulungu walepheretsa zimene iwowo adaapangana kuti atichite. Tsono tonse tidapitanso ku ntchito yomanga khoma, aliyense ku ntchito yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti chinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pachabe uphungu wao, tinabwera tonse kunka kulinga, yense kuntchito yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adani athu atamva kuti ife tadziwa za chiwembu chawo, anadziwanso kuti Yehova walepheretsa zimene ankafuna kutichita. Choncho tinabwerera aliyense ku ntchito yake yomanga khoma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali, pakumva adani athu kuti cinadziwika nafe, ndi kuti Mulungu adapititsa pacabe uphungu wao, tinabwera tonse kumka kulinga, yense ku nchito yace.