Nehemiah 4:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, theka lina la antchito anga linkagwira ntchitoyo, ndipo theka lina linkagwira mikondo, zishango, mauta ndiponso linkavala malaya achitsulo. Tsono akulu a Ayuda ankalimbitsa anthu ao amene ankamanga khoma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira ntchito, ndi gawo lina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi malaya achitsulo; ndi akulu anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo mwake, theka la antchito anga linkagwira ntchito, pamene theka linalo limatenga mikondo, zishango, mauta ndi kuvala malaya azitsulo. Akuluakulu ankalimbikitsa Ayuda onse
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kuyambira pamenepo gawo lina la anyamata anga anagwira nchito, ndi gawo ina linagwira nthungo, zikopa, ndi mauta, ndi maraya acitsulo; ndi akuru anali m'mbuyo mwa nyumba yonse ya Yuda.