Nehemiah 4:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mmisiri aliyense anali atamangirira lupanga m'chiwuno mwake pamene ankamanga. Munthu woimba lipenga anali pambali panga nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi omanga linga aliyense anamangirira lupanga lake m'chuuno mwake, nagwira ntchito motero. Ndipo woomba lipenga anali ndi ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmisiri aliyense ankamangirira lupanga lake mʼchiwuno mwake akamagwira ntchito. Koma munthu woyimba lipenga anali pambali panga nthawi zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi omanga linga ali yense anamangirira lupanga lace m'cuuno mwace, nagwira nchito motero. Ndipo woomba lipenga anali ndi ine.