Nehemiah 4:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalankhula pamaso pa abale ake, ndi pamaso pa gulu lankhondo la ku Samariya, adati, “Kodi Ayuda achabechabeŵa akuchita chiyani? Monga amati nkumanganso mzindawu? Kodi nsembe ndiye adzapereka? Kodi adzaumaliza pa tsiku limodzi? Kodi adzachita kutolatolanso miyala yakale ija, ndi m'mene idapsera muja?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anayankhula pamaso pa abale ake ndi asilikali a Samariya kuti, “Kodi Ayuda ofowokawa akuchita chiyani? Kodi iwo nʼkumanganso khoma? Kodi adzaperekanso nsembe? Kodi adzatsiriza ntchitoyi tsiku limodzi? Kodi adzachita kutenga miyala yakale ija ndi mmene inapseramo?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanena iye pamaso pa abale ace ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikucitanji Ayuda ofokawa? adzimangire linga kodi? adzapereka nsembe kodi? adzatsiriza tsiku limodzi kodi? adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?