Nehemiah 4:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imeneyi ndidaŵauzanso anthu kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone m'Yerusalemu, kuti tikhale ndi otitchinjiriza usiku, ndipo kuti masana tizigwira ntchito.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Aliyense agone m'Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wake, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira ntchito usana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo ndinawuzanso anthuwo kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone mu Yerusalemu kuti tikhale ndi otilondera usiku ndi kuti masana tizigwira ntchito.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinanenanso kwa anthu nthawi yomweyi, Ali yense agone m'Yerusalemu pamodzi ndi mnyamata wace, kuti atilindirire usiku, ndi kugwira nchito usana.