Nehemiah 4:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma pamene Sanibalati ndi Tobiya, ndiponso Arabu, Aamoni ndi Aasidodi adamva kuti ntchito yokonza makoma a Yerusalemu ikupita m'tsogolo, ndipo kuti malo ogamukagamuka aja akuŵakonzanso, adapsa mtima kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwake munayamba kutsekeka, chidawaipira kwambiri;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pamene Sanibalati, Tobiya, Aarabu, Aamoni ndi anthu a ku Asidodi anamva kuti ntchito yokonzanso makoma a Yerusalemu ikupitirirabe ndipo kuti mipata ikutsekedwa, anapsa mtima kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kunali, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Aarabu, ndi Aamoni, ndi Aasidodi, kuti makonzedwe a malinga a Yerusalemu anakula, ndi kuti mopasuka mwace munayamba kutsekeka, cidawaipira kwambiri;