Nehemiah 5:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muŵabwezere lero lomwe lino minda yao, mitengo yao yamphesa, mitengo yao ya olivi, ndi nyumba zao, ndipo muŵakhululukire ngongole za ndalama, za tirigu, za vinyo, ndi za mafuta, zimene mudaaŵakongoza.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abwezereni lero lomwe minda yawo, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndiponso nyumba zawo. Muwabwezerenso chiwongoladzanja cha ndalama, tirigu, vinyo ndi mafuta zimene munatenga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao yaazitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndarama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.