Nehemiah 5:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambiranso nthaŵi imene adandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa m'dziko la Yuda, kuchokera chaka cha 20 mpaka chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, ndiye kuti zaka khumi ndi ziŵiri, ineyo ndi abale anga sitidalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadya chakudya cha kazembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso kuyambira nthawi imene anandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda, kuchokera chaka cha makumi awiri mpaka chaka cha 32 muulamuliro wa ufumu wa Aritasasita, ndiye kuti kwa zaka zokwana 12, ine ngakhale abale anga sitinalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ciyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira caka ca makumi awiri kufikira caka ca makumi atatu mphambu ziwiri ca Aritasasta mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadya cakudya ca kazembe.