Nehemiah 5:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abwanamkubwa amene analipo kale ankasautsa anthu pomaŵalanda chakudya ndi vinyo, ndi kuŵalipitsanso masekeli asiliva makumi anai. Ngakhale antchito ao nawonso ankathinitsa anthu. Koma ine sindidachite nawo zimenezo, popeza kuti ndinkaopa Mulungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma abwanamkubwa akale ankasautsa anthu. Iwo ankalanda anthu chakudya ndi vinyo ndi kuwalipiritsanso masekeli asiliva makumi anayi. Ngakhalenso antchito awo amavutitsa anthu kwambiri. Koma ine sindinachite zimenezo chifukwa ndimaopa Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakale anyamata ao anacita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, cifukwa ca kuopa Mulungu.