Nehemiah 5:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiponso ndinkakangamira pa ntchito yomanga makoma a mzinda, osafuna kupata minda. Antchito anga onsenso anali komweko, ndidaaŵalamula kuti adzipereke pa ntchito yokhayokhayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligula, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndiponso ndinadzipereka kugwira ntchito yomanga khoma la mzinda wa Yerusalemu popanda ngakhale kugulapo munda. Antchito anganso anasonkhana komweko kuti agwire ntchito ndipo sitinafunenso malo ena.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso ndinalimbikira nchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligula, ndi anyamata anga onse anasonkhanira nchito komweko.