Nehemiah 5:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono chakudya cha pa tsiku limodzi chinali ichi: ng'ombe imodzi, nkhosa zisanu ndi imodzi zonenepa, ndiponso nkhuku zochuluka. Pa masiku khumi aliwonse panalinso matumba achikopa ochuluka a vinyo. Komabe ngakhale choncho, ine sindidafune kulandira chakudya chimene abwanamkubwa ankalandira, chifukwa chakuti anthu anga anali othinidwa kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundumitundu; chinkana chonsechi sindinafunsira chakudya cha kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lililonse pamaphikidwa ngʼombe imodzi, nkhosa zabwino zisanu ndi imodzi pamodzi ndi nkhuku. Ndipo pakutha pa masiku khumi aliwonse pankakhala matumba achikopa ochuluka a vinyo wa mitundu yonse. Ngakhale zinali choncho, Ine sindinatenge chakudya choperekedwa kwa bwanamkubwa, chifukwa izi zinali zosautsa anthu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zokonzekeratu tsiku limodzi tsono ndizo ng'ombe imodzi, ndi nkhosa zonenepa zisanu ndi imodzi, anandikonzeratunso nkhuku, ndi kamodzi atapita masiku khumi vinyo wambiri wa mitundu mitundu; cinkana conseci sindinafunsira cakudya ca kazembe, popeza ukapolo unalemerera anthuwo.