Nehemiah 5:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidatsimikiza kuti ndichitepo kanthu, ndipo ndidaŵadzudzula atsogoleri ndi akulu olamula omwe. Ndidati, “Kodi nzokuwonerani kuti mukulipitsana chiwongoladzanja anthu apachibale nokhanokha!” Pamenepo ndidachititsa msonkhano waukulu kuti ndiŵazenge mlandu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufulu ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wake. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukulu wakuwatsutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nditalingalira bwino ndinatsimikiza zoti ndichitepo kanthu ndipo kenaka ndinawadzudzula anthu olemekezeka ndi akuluakuluwo. Ndinawawuza kuti, “Zoona ndithu inu nʼkumalipiritsana chiwongoladzanja chachikulu anthu apachibale nokhanokha!” Choncho ndinayitanitsa msonkhano waukulu kuti ndiwazenge mlandu
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo mtima wanga unandipangira; ndipo ndinatsutsana nao aufuru ndi olamulira, ndi kunena nao, Mukongoletsa mwa phindu yense kwa mbale wace. Ndipo ndinasonkhanitsa msonkhano waukuru wakuwatsutsa.